-
Yeremiya 23:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
“Musamvere mawu a aneneri amene akulosera kwa inu.+
Iwo akungokupusitsani.*
17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti,
‘Yehova wanena kuti: “Inu mudzakhala pa mtendere.”’+
Ndipo aliyense amene amatsatira mtima wake woipawo akumuuza kuti,
‘Tsoka silidzakugwerani.’+
-
-
Ezekieli 13:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kodi masomphenya amene mwaonawa si abodza ndipo zimene mwaloserazi si zonama pamene mukunena kuti, ‘Yehova wanena kuti,’ pamene ine sindinanene chilichonse?”’
-