-
Oweruza 17:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Choncho anabweza ndalama zasiliva zokwana 1,100 zija kwa mayi ake. Koma mayi akewo anati: “Ndalamazi ndizipereka kwa Yehova kuti zikhale zopatulika. Ndikufuna kuti iweyo ugwiritse ntchito ndalamazi kukapangitsa chifaniziro chosema ndiponso chifaniziro chachitsulo.+ Choncho ndikukupatsa ndalamazi.”
4 Mika atabweza ndalamazo kwa mayi ake, mayi akewo anatenga ndalama zasiliva 200 nʼkuzipereka kwa wosula siliva. Wosula silivayo anapanga zifaniziro ziwiri. Zifanizirozi anaziika mʼnyumba ya Mika.
-