Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 16:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Muzisangalala pa chikondwerero chimenecho,+ inuyo, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, Mlevi, mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye, amene ali mumzinda wanu.

  • Salimo 42:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Ndikukumbukira zinthu zimenezi ndipo mtima wanga ukupweteka kwambiri.

      Chifukwa poyamba ndinkayenda ndi gulu lalikulu la anthu,

      Ndinkayenda pangʼonopangʼono patsogolo pawo kupita kunyumba ya Mulungu,

      Gulu la anthu likuimba mosangalala nyimbo zoyamika Mulungu,

      Pa nthawi ya chikondwerero.+

  • Yeremiya 33:10, 11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Yehova wanena kuti: ‘Pamalo ano amene mudzanene kuti ndi bwinja, opanda anthu kapena ziweto, mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu imene yawonongeka, moti mulibe anthu ndipo simukukhala aliyense ngakhale ziweto, mʼmalo amenewa mudzamveka 11 phokoso la chikondwerero ndi chisangalalo.+ Mudzamvekanso mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi komanso mawu a anthu amene akunena kuti: “Yamikani Yehova wa magulu ankhondo akumwamba chifukwa Yehova ndi wabwino+ ndipo chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale!”’+

      ‘Anthuwo adzabweretsa nsembe zoyamikira kunyumba ya Yehova,+ chifukwa ndidzabwezeretsa anthu amʼdzikoli, amene anatengedwa kupita kudziko lina, kuti akhalenso ngati mmene analili poyamba,’ akutero Yehova.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena