37 Choncho Senakeribu mfumu ya Asuri anachoka nʼkubwerera kukakhala ku Nineve.+ 38 Pamene Senakeribu ankaweramira mulungu wake Nisiroki mʼkachisi, ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga+ nʼkuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako mwana wake Esari-hadoni+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.