24 Mʼmalo mwa mafuta onunkhira a basamu+ padzangokhala fungo loipa.
Mʼmalo mwa lamba padzakhala chingwe.
Mʼmalo mwa tsitsi lokonzedwa bwino padzakhala mpala.+
Mʼmalo mwa chovala chamtengo wapatali adzavala chiguduli,+
Ndipo padzakhala chipsera mʼmalo mwa kukongola.