9 Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu,+ nyumba ya munthu aliyense wotchuka+ komanso nyumba zonse za mu Yerusalemu.+ 10 Kenako asilikali onse a Akasidi, omwe anali ndi mkulu wa asilikali olondera mfumu uja, anagwetsa mpanda wonse wa Yerusalemu.+