-
2 Mbiri 31:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Atangomaliza kuchita zonsezi, Aisiraeli onse amene anali pamenepo anapita kumizinda ya Yuda nʼkukaphwanya zipilala zopatulika,+ kugwetsa mizati yopatulika,*+ malo okwezeka+ ndiponso maguwa ansembe+ mʼmadera onse a Yuda, Benjamini, Efuraimu ndi Manase+ mpaka kuzimaliza zonse. Atatero, Aisiraeli anabwerera kumizinda yawo, aliyense kumalo ake.
-