-
2 Mafumu 18:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Atamva zimenezi, Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina+ ndi Yowa anauza Rabisake+ kuti: “Chonde lankhulani ndi ife atumiki anu mʼchilankhulo cha Chiaramu*+ chifukwa timachimva. Musalankhule nafe mʼchilankhulo cha Ayuda, kuti anthu amene ali pamakomawa asamve.”+ 27 Koma Rabisake anawayankha kuti: “Kodi mbuye wanga wandituma kuti uthengawu ndidzauze mbuye wanu ndi inuyo basi? Kodi sananditumenso kwa amuna amene akhala pamakomawo, amene adzadye chimbudzi chawo ndi kumwa mkodzo wawo limodzi ndi inuyo?”
-