2 Mafumu 17:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Mʼchaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ nʼkutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani+ ndiponso mʼmizinda ya Amedi.+ 2 Mafumu 17:22, 23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Aisiraeli anapitiriza kuyenda mʼmachimo onse amene Yerobowamu anachita.+ Sanawasiye 23 mpaka Yehova anachotsa Aisiraeli pamaso pake ngati mmene ananenera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri.+ Choncho Aisiraeli anatengedwa mʼdziko lawo nʼkupita nawo ku Asuri+ ndipo ali komweko mpaka lero. Yesaya 10:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Kodi zimene ndachitira Samariya ndi milungu yake yopanda phindu,+Si zimenenso ndidzachitire Yerusalemu ndi mafano ake?’
6 Mʼchaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ nʼkutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani+ ndiponso mʼmizinda ya Amedi.+
22 Aisiraeli anapitiriza kuyenda mʼmachimo onse amene Yerobowamu anachita.+ Sanawasiye 23 mpaka Yehova anachotsa Aisiraeli pamaso pake ngati mmene ananenera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri.+ Choncho Aisiraeli anatengedwa mʼdziko lawo nʼkupita nawo ku Asuri+ ndipo ali komweko mpaka lero.
11 Kodi zimene ndachitira Samariya ndi milungu yake yopanda phindu,+Si zimenenso ndidzachitire Yerusalemu ndi mafano ake?’