-
Hoseya 11:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Kodi ndikusiye chifukwa chiyani iwe Efuraimu?+
Kodi ndikupereke kwa adani chifukwa chiyani iwe Isiraeli?
Kodi ndikuchitire zinthu ngati Adima chifukwa chiyani?
Kodi ndikusinthirenji kukhala ngati Zeboyimu?+
Koma ndasintha maganizo
Ndipo ndayamba kukumvera chisoni.+
9 Sindidzasonyeza mkwiyo wanga woyaka moto.
Sindidzawononganso Efuraimu+
Chifukwa ndine Mulungu, osati munthu.
Ndine Woyera pakati panu,
Ndipo sindidzabwera kwa inu nditakwiya.
-