22 Ndiyeno Mfumu Asa inaitanitsa Ayuda onse moti palibe amene anatsala, ndipo iwo anatenga miyala ndi matabwa za ku Rama zimene Basa ankamangira. Mfumu Asa anatenga zinthu zimenezi nʼkukamangira mzinda wa Geba+ ku Benjamini ndi wa Mizipa+ kuti mizindayi ikhale yolimba.