-
2 Mafumu 25:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Mʼmwezi wa 5, pa tsiku la 7 la mweziwo, chomwe chinali chaka cha 19 cha Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo, Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, mtumiki wa mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu.+ 9 Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu,+ nyumba ya munthu aliyense wotchuka+ komanso nyumba zonse za mu Yerusalemu.+ 10 Kenako asilikali onse a Akasidi, omwe anali ndi mkulu wa asilikali olondera mfumu uja, anagwetsa mpanda wonse wa Yerusalemu.+
-
-
2 Mbiri 34:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 “Yehova wanena kuti, ‘Ndibweretsa tsoka pamalo ano ndiponso kwa anthu ake,+ pokwaniritsa matemberero onse amene analembedwa mʼbuku+ limene anawerenga pamaso pa mfumu ya Yuda, 25 chifukwa chakuti andisiya+ nʼkumakapereka nsembe zautsi kwa milungu ina kuti andikwiyitse+ ndi ntchito zonse za manja awo, ndibweretsa mkwiyo wanga pamalo ano ndipo suzimitsidwa.’”+
-
-
2 Mbiri 36:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Koma iwo anapitiriza kunyoza atumiki a Mulungu woona,+ kunyoza mawu ake+ ndiponso kuseka aneneri ake.+ Iwo anafika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa. Kenako Yehova anawakwiyira kwambiri nʼkuwalanga.+
17 Choncho anawabweretsera mfumu ya Akasidi+ yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga+ mʼnyumba yopatulika.+ Sinamvere chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena wodwala.+ Mulungu anapereka zonse mʼmanja mwake.+
-