Yeremiya 38:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Akalonga anauza mfumu kuti: “Chonde lamulani kuti munthu uyu aphedwe+ chifukwa akufooketsa asilikali amene atsala mumzinda uno komanso anthu onse, powauza mawu amenewa. Munthu ameneyu sakuwafunira mtendere anthuwa, koma akuwafunira tsoka.” Yeremiya 38:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Choncho iwo anagwira Yeremiya nʼkumuponya mʼchitsime cha Malikiya mwana wa mfumu, chimene chinali mʼBwalo la Alonda.+ Iwo analowetsa Yeremiya mʼchitsimemo pogwiritsa ntchito zingwe. Mʼchitsimemo munalibe madzi koma munali matope ndipo Yeremiya anayamba kumira mʼmatopemo.
4 Akalonga anauza mfumu kuti: “Chonde lamulani kuti munthu uyu aphedwe+ chifukwa akufooketsa asilikali amene atsala mumzinda uno komanso anthu onse, powauza mawu amenewa. Munthu ameneyu sakuwafunira mtendere anthuwa, koma akuwafunira tsoka.”
6 Choncho iwo anagwira Yeremiya nʼkumuponya mʼchitsime cha Malikiya mwana wa mfumu, chimene chinali mʼBwalo la Alonda.+ Iwo analowetsa Yeremiya mʼchitsimemo pogwiritsa ntchito zingwe. Mʼchitsimemo munalibe madzi koma munali matope ndipo Yeremiya anayamba kumira mʼmatopemo.