Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 25:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho ndinatenga kapu imene inali mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse imene Yehova ananditumizako. Mitunduyo ndi iyi:+

  • Yeremiya 25:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 ndiponso anthu a mitundu yosiyanasiyana. Mafumu onse amʼdziko la Uzi, mafumu onse amʼdziko la Afilisiti,+ Asikeloni,+ Gaza, Ekironi komanso amene anatsala ku Asidodi,

  • Ezekieli 25:15, 16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Popeza Afilisiti akupitiriza kuchitira zoipa Aisiraeli chifukwa chodana nawo, iwo akufuna kubwezera komanso kuwononga Aisiraeliwo mwankhanza.*+ 16 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikutambasula dzanja langa kuti ndilange Afilisiti,+ ndipo ndidzapha Akereti+ nʼkuwononga anthu onse omwe anatsala, amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.+

  • Amosi 1:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Yehova wanena kuti,

      ‘“Chifukwa chakuti Gaza+ wandigalukira mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa.

      Chifukwa anatenga anthu onse ogwidwa ukapolo+ nʼkuwapereka ku Edomu.

  • Zefaniya 2:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Gaza adzakhala mzinda wosiyidwa,

      Ndipo Asikeloni adzakhala bwinja.+

      Anthu a ku Asidodi adzathamangitsidwa dzuwa likuswa mtengo,*

      Ndipo Ekironi adzazulidwa.+

  • Zekariya 9:5, 6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Asikeloni adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha.

      Gaza adzamva ululu waukulu.

      Izi zidzachitikiranso Ekironi chifukwa amene ankamudalira wachititsidwa manyazi.

      Ku Gaza sikudzakhalanso mfumu,

      Ndipo ku Asikeloni sikudzakhalanso anthu.+

       6 Mwana wochokera mu mtundu wina wa anthu azidzakhala ku Asidodi,

      Ndipo ndidzathetsa kunyada kwa Afilisiti.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena