Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 23:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Uwu ndi uthenga wokhudza Turo:+

      Lirani mofuula inu sitima zapamadzi za ku Tarisi,+

      Chifukwa chakuti doko lawonongedwa ndipo simungathenso kufikapo.

      Anthu amva zimenezi ali kudziko la Kitimu.+

  • Yesaya 23:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Chita manyazi iwe Sidoni, iwe mzinda wotetezeka umene uli mʼmbali mwa nyanja,

      Chifukwa nyanja yanena kuti:

      “Sindinamvepo zowawa zapobereka, ndipo sindinaberekepo,

      Komanso sindinalerepo anyamata kapena atsikana.”*+

  • Yeremiya 25:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho ndinatenga kapu imene inali mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse imene Yehova ananditumizako. Mitunduyo ndi iyi:+

  • Yeremiya 25:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 mafumu onse a Turo, mafumu onse a Sidoni+ ndi mafumu a pachilumba chamʼnyanja.

  • Yeremiya 27:2, 3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Yehova wandiuza kuti, ‘Upange zomangira komanso magoli ndipo uzivale mʼkhosi mwako. 3 Kenako uzitumize kwa mfumu ya Edomu,+ mfumu ya Mowabu,+ mfumu ya Aamoni,+ mfumu ya Turo+ ndi mfumu ya Sidoni.+ Upatsire amithenga amene abwera ku Yerusalemu kudzaonana ndi Zedekiya mfumu ya Yuda.

  • Ezekieli 28:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana ku Sidoni+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzamuchitikire.

  • Yoweli 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Komanso kodi ndakulakwira chiyani

      Iwe Turo ndi Sidoni ndiponso nonse amʼchigawo cha Filisitiya?

      Kodi mukundichitira zimenezi pondibwezera zimene ndinachita?

      Ngati mukundibwezera,

      Ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena