-
2 Mafumu 24:17-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Mfumu ya Babulo inatenga Mataniya, bambo ake aangʼono a Yehoyakini,+ nʼkuwaika kukhala mfumu mʼmalo mwake. Kenako inawasintha dzina kuti akhale Zedekiya.+
18 Zedekiya anayamba kulamulira ali ndi zaka 21 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya. 19 Zedekiya ankachita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehoyakimu anachita.+ 20 Zinthu zimenezi zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda chifukwa Yehova anakwiya kwambiri mpaka anawachotsa pamaso pake.+ Kenako Zedekiya anagalukira mfumu ya Babulo.+
-