24Mʼmasiku a Yehoyakimu, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera kudzamenyana naye. Ndipo Yehoyakimu anakhala mtumiki wake kwa zaka zitatu, koma kenako anamugalukira.
5 Yehoyakimu+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 25 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.+