Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 18:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Nʼchifukwa chake dzikolo ndi lodetsedwa, ndipo ndidzalilanga chifukwa cha zolakwa zake moti dzikolo lidzalavula anthu ake kunja.+

  • Levitiko 26:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukuthamangitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja, ndipo mizinda yanu idzawonongedwa.+

  • Deuteronomo 28:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Yehova adzakuthamangitsani limodzi ndi mfumu yanu imene mudzaike kuti izikulamulirani, kukupititsani ku mtundu umene inuyo kapena makolo anu sanaudziwe.+ Kumeneko mudzatumikira milungu ina, milungu yamtengo ndi yamwala.+

  • Yesaya 24:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Anthu onse adzachotsedwa mʼdzikolo.

      Katundu yense wamʼdzikolo adzatengedwa,+

      Chifukwa Yehova ndi amene wanena mawu amenewa.

  • Yeremiya 25:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 ndikuitana mafuko onse akumpoto,”+ akutero Yehova, “ndikuitananso Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo, mtumiki wanga.+ Ndibweretsa anthu amenewa kuti aukire dziko lino+ ndi anthu amene akukhala mmenemo komanso mitundu yonse imene yakuzungulirani.+ Ndidzakuwonongani inuyo ndi mitundu yonse yokuzungulirani ndipo ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha chimene anthu azidzachiimbira mluzu ndipo malo anu adzakhala mabwinja mpaka kalekale.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena