-
Yeremiya 28:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Kenako mneneri Yeremiya anauza mneneri Hananiya+ kuti: “Tamvera iwe Hananiya! Yehova sanakutume, koma iwe wachititsa anthuwa kukhulupirira zinthu zabodza.+ 16 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Ndikukuchotsera moyo wako. Chaka chomwe chino iweyo ufa, chifukwa walimbikitsa anthu kuti apandukire Yehova.’”+
-
-
Ezekieli 13:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘Chifukwa choti mwalankhula zabodza ndipo masomphenya anu ndi onama, ine ndithana nanu,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+ 9 Dzanja langa likulimbana ndi aneneri amene masomphenya awo ndi abodza ndiponso amene akulosera zonama.+ Iwo sadzakhala mʼgulu la anthu amene ndimawakonda ndipo sadzalembedwa mʼbuku la mayina a anthu a nyumba ya Isiraeli. Komanso sadzabwerera kudziko la Isiraeli ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+
-