-
Yeremiya 30:18, 19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Yehova wanena kuti:
“Ndikusonkhanitsa anthu amʼmatenti a Yakobo amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,+
Ndipo ndidzamvera chisoni malo okhala a Yakobo.
Mzinda udzamangidwanso pamalo amene unali poyamba,+
Ndipo nsanja yokhala ndi mpanda wolimba idzakhala pamalo ake oyenerera.
19 Kwa iwo kudzamveka mawu oyamikira ndi phokoso la kuseka kwa anthu.+
-