27 ‘Koma iwe Yakobo mtumiki wanga, usaope
Ndipo usachite mantha, iwe Isiraeli.+
Chifukwa ndidzakupulumutsa kuchokera kutali.
Ndipo ndidzapulumutsa mbadwa yako kuchokera mʼdziko limene anali kapolo.+
Yakobo adzabwerera nʼkukhala mwamtendere ndiponso mosatekeseka,
Sipadzakhala wowaopseza.+