-
Ezekieli 18:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Kodi mwambi umene mumanena mʼdziko la Isiraeli wakuti, ‘Bambo adya mphesa zosapsa koma mano a ana ndi amene ayezimira,’+ umatanthauza chiyani?
3 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, simudzanenanso mwambi umenewu mu Isiraeli. 4 Tamverani! Miyoyo yonse ndi yanga. Moyo wa bambo komanso moyo wa mwana, yonse ndi yanga. Moyo umene wachimwa ndi umene udzafe.*
-