-
Aheberi 8:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 “‘Pangano limene ndidzapangane ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa masiku amenewo ndi ili: Ndidzaika malamulo anga mʼmaganizo mwawo ndiponso kuwalemba mʼmitima yawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga,’+ akutero Yehova.*
11 ‘Munthu sadzaphunzitsanso nzika inzake kapena mʼbale wake kuti, “Mumʼdziwe Yehova!”* Chifukwa aliyense adzandidziwa kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. 12 Ine ndidzawachitira chifundo pa zochita zawo zosalungama, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.’”+
-