Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 5:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Aneneri akulosera zabodza,+

      Ndipo ansembe akugwiritsa ntchito mphamvu zawo kuti azilamulira ena.

      Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+

      Koma kodi mudzachita chiyani mapeto akadzafika?”

  • Yeremiya 14:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera zinthu zabodza mʼdzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo ndi masomphenya abodza, maulosi opanda pake ndi chinyengo chamumtima mwawo.+

  • Mika 3:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Atsogoleri amumzindawo saweruza asanalandire ziphuphu,+

      Ansembe ake amaphunzitsa kuti apeze malipiro,+

      Ndipo aneneri ake amalosera kuti apeze ndalama.+

      Komatu iwo amanena kuti amadalira Yehova ndipo amati:

      “Yehovatu ali nafe,+

      Ndipo tsoka silidzatigwera.”+

  • Zefaniya 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Aneneri ake ndi amwano ndiponso achinyengo.+

      Ansembe ake amaipitsa zinthu zopatulika,+

      Ndipo amaphwanya malamulo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena