14 Mfumuyo inatenga anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ asilikali onse amphamvu, amisiri onse ndiponso anthu osula zitsulo+ nʼkupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu osauka kwambiri a mʼdzikolo.+