-
Yesaya 66:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Ndidzaika chizindikiro pakati pawo ndipo ena mwa anthu amene adzapulumuke ndidzawatumiza ku mitundu ya anthu. Ndidzawatumiza kwa anthu aluso lokoka uta omwe ndi a ku Tarisi,+ ku Puli ndi ku Ludi.+ Ndidzawatumizanso kwa anthu a ku Tubala ndi ku Yavani+ komanso akuzilumba zakutali amene sanamvepo zokhudza ine kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalengeza za ulemerero wanga pakati pa mitundu ya anthu.+
-