-
Zefaniya 3:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Yehova wanena kuti: ‘Choncho pitirizani kundiyembekezera,*+
Mpaka tsiku limene ndidzanyamuke kuti ndikatenge zinthu za anthu omwe ndawagonjetsa.*
Chiweruzo changa ndi choti ndisonkhanitse mitundu ya anthu, ndisonkhanitse maufumu,
Kuti ndiwasonyeze mkwiyo wanga, ndithu mkwiyo wanga wonse woyaka moto,+
Chifukwa moto wa mkwiyo wanga udzawotcheratu dziko lonse lapansi.+
-