2 Ndidzasonkhanitsanso anthu a mitundu yonse,
Nʼkuwabweretsa mʼchigwa cha Yehosafati.
Ndipo ndidzawaweruza kumeneko,+
Mʼmalo mwa anthu anga ndiponso cholowa changa, Isiraeli.
Chifukwa anamwaza Aisiraeli pakati pa anthu a mitundu ina,
Ndiponso anagawana dziko langa.+