-
2 Mafumu 23:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Kenako inaitanitsa ansembe onse kuchokera mʼmizinda ya Yuda. Ndipo malo okwezeka amene ansembewo ankaperekako nsembe yautsi, kuyambira ku Geba+ mpaka ku Beere-seba,+ inawachititsa kuti akhale osayenera kulambirako. Inagwetsanso malo okwezeka a pageti amene anali pakhomo lapageti la Yoswa mkulu wa mzindawo. Getilo linali mbali ya kumanzere munthu akamalowa pageti la mzindawo. 9 Ansembe a malo okwezekawo sankatumikira kuguwa lansembe la Yehova ku Yerusalemu.+ Koma ankadya mikate yopanda zofufumitsa limodzi ndi abale awo.
-
-
Nehemiya 9:34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Mafumu athu, akalonga athu, ansembe athu ndi makolo athu sanatsatire Chilamulo chanu ndipo sanamvere malamulo anu kapena zikumbutso zanu zowachenjeza.
-
-
Ezekieli 8:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Kenako iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kweza maso ako uyangʼane kumpoto.” Choncho ndinakweza maso anga nʼkuyangʼana kumpoto, ndipo ndinaona kuti kumpoto kwa geti la guwa lansembe kunali fano loimira nsanje lija pakhomo la getilo.
-