12 Iwo anaumitsa mtima wawo ngati mwala wa dayamondi+ ndipo sanamvere malamulo ndi mawu a Yehova wa magulu ankhondo akumwamba amene anawatumizira pogwiritsa ntchito mzimu wake kudzera mwa aneneri akale.+ Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba anakwiya kwambiri.”+