-
Yeremiya 52:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo nʼkupita nayo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo mʼdziko la Hamati ndipo anaipatsa chigamulo.
-
-
Ezekieli 17:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Ndidzamuponyera ukonde wanga ndipo adzakodwa mu ukonde wanga wosakira.+ Ndiyeno ndidzamubweretsa ku Babulo nʼkumuweruza chifukwa chondichitira zinthu mosakhulupirika.+ 21 Asilikali ake onse amene anathawa adzaphedwa ndi lupanga ndipo amene adzapulumuke adzabalalikira kumbali zonse.*+ Zikadzatero mudzadziwa kuti ine Yehova ndi amene ndanena zimenezi.”’+
-