16 Ulemerero wa Yehova+ unakhalabe paphiri la Sinai,+ ndipo mtambowo unakuta phirilo kwa masiku 6. Pa tsiku la 7, Mulungu anaitana Mose kuchokera mumtambowo. 17 Kwa Aisiraeli amene ankaona zimenezi, ulemerero wa Yehova unkaoneka ngati moto wolilima pamwamba pa phiri.