18 “Iwe mwana wa munthu, lirira gulu la anthu onse a ku Iguputo ndipo utsitsire dzikolo kumanda. Utsitsire kumanda dzikolo ndi ana aakazi a mitundu yamphamvu limodzi ndi amene akutsikira kudzenje.*
20 Iguputo adzaphedwa pamodzi ndi anthu amene aphedwa ndi lupanga.+ Iye adzaphedwa ndi lupanga. Mukokereni kutali limodzi ndi gulu la anthu ake onse amene amamutsatira.