Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 8:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Kenako tinapereka malamulo a mfumu+ kwa masatarapi* a mfumu ndi abwanamkubwa a kutsidya lina la Mtsinje.*+ Malamulowo anathandiza anthuwo ndiponso anathandiza panyumba ya Mulungu woona.+

  • Esitere 8:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Choncho pa nthawiyi anaitana alembi a mfumu. Limeneli linali tsiku la 23 la mwezi wachitatu womwe ndi mwezi wa Sivani.* Iwo analemba zonse zimene Moredikayi analamula Ayuda kuti achite. Makalatawo analinso opita kwa masatarapi,*+ abwanamkubwa ndi akalonga amʼzigawo zonse+ kuchokera ku Indiya mpaka ku Itiyopiya, zigawo 127. Chigawo chilichonse anachilembera mogwirizana ndi kalembedwe ka anthu akumeneko ndiponso chilankhulo chawo. Nawonso Ayuda anawalembera mogwirizana ndi kalembedwe kawo ndiponso chilankhulo chawo.

  • Danieli 3:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Kenako Mfumu Nebukadinezara inatumiza uthenga kwa masatarapi,* akuluakulu a boma, abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu a zamalamulo ndi oyangʼanira onse a zigawo kuti asonkhane kumwambo wotsegulira fano limene Mfumu Nebukadinezara inaimika.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena