-
Danieli 6:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Koma Danieli atangodziwa kuti lamulo limeneli lasainidwa, anapita kunyumba kwake. Mawindo a chipinda chake chamʼmwamba anali otsegula ndipo anayangʼana ku Yerusalemu.+ Katatu pa tsiku, iye ankagwada nʼkupemphera kwa Mulungu wake komanso kumutamanda, ngati mmene ankachitira nthawi zonse lamuloli lisanasainidwe.
-