4 Ine Nebukadinezara ndinkakhala mwabata mʼnyumba mwanga ndipo zinthu zinkandiyendera bwino mʼnyumba yanga yachifumu. 5 Ndiyeno ndinalota maloto amene anandichititsa mantha. Nditagona pabedi langa ndinaona zithunzithunzi ndi masomphenya zimene zinandichititsa mantha.+