-
Danieli 4:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Choncho ndinalamula kuti amuna onse anzeru a mʼBabulo awabweretse kwa ine kuti adzandimasulire malotowo.+
7 Pa nthawi imeneyo ansembe ochita zamatsenga, anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi okhulupirira nyenyezi+ anabwera kwa ine. Nditawafotokozera malotowo, sanathe kundiuza kumasulira kwake.+
-
-
Danieli 5:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ndiye mfumuyo inaitana mofuula olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi okhulupirira nyenyezi.+ Mfumuyo inauza amuna anzeru a mʼBabulo amenewa kuti: “Aliyense amene angawerenge mawuwa nʼkundiuza kumasulira kwake, ndimuveka zovala zapepo ndi mkanda wagolide mʼkhosi+ ndipo akhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”+
8 Amuna onse anzeru anabwera kwa mfumu koma sanathe kuwerenga mawu amene analembedwawo kapena kuuza mfumu kumasulira kwake.+
-