-
Danieli 8:23, 24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Kumapeto kwa ufumu wawo, zochita za anthu ochimwawo zikadzafika pachimake, mfumu yooneka mochititsa mantha ndiponso yomvetsa zinthu zovuta kumva idzayamba kulamulira. 24 Mphamvu za mfumuyo zidzachuluka, koma si iye amene adzachititse zimenezi. Idzawononga zinthu zambiri moti idzadabwitsa anthu. Chilichonse chimene mfumuyo izidzachita chizidzaiyendera bwino. Idzawononga anthu amphamvu ndi anthu oyera.+
-
-
Danieli 12:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kenako ndinamva munthu amene anavala nsalu uja, amene anali pamwamba pa madzi amumtsinje akuyankha. Iye anakweza mʼmwamba dzanja lake lamanja ndi lamanzere nʼkulumbira pa Mulungu amene adzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ ndipo anati: “Padzadutsa nthawi imodzi yoikidwiratu, nthawi ziwiri zoikidwiratu ndi hafu ya nthawi yoikidwiratu.* Ndipo akadzangomaliza kuphwanyaphwanya mphamvu za anthu oyera,+ zinthu zonsezi zidzafika pamapeto.”
-