-
Danieli 12:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Kenako ndinamva munthu amene anavala nsalu uja, amene anali pamwamba pa madzi amumtsinje akuyankha. Iye anakweza mʼmwamba dzanja lake lamanja ndi lamanzere nʼkulumbira pa Mulungu amene adzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ ndipo anati: “Padzadutsa nthawi imodzi yoikidwiratu, nthawi ziwiri zoikidwiratu ndi hafu ya nthawi yoikidwiratu.* Ndipo akadzangomaliza kuphwanyaphwanya mphamvu za anthu oyera,+ zinthu zonsezi zidzafika pamapeto.”
-
-
Chivumbulutso 13:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Chilombocho chinapatsidwa pakamwa polankhula zinthu zodzitukumula ndi zonyoza Mulungu. Chinapatsidwanso mphamvu yochita zimene chikufuna kwa miyezi 42.+ 6 Chilombocho chinatsegula pakamwa pake nʼkumanyoza+ Mulungu. Chinkanyoza dzina lake, malo ake okhala komanso amene akukhala kumwamba.+ 7 Chinaloledwa kumenyana ndi oyerawo nʼkuwagonjetsa.+ Chinapatsidwanso ulamuliro pa anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, chilankhulo chilichonse ndi dziko lililonse.
-