8 Ndiyeno anthu atalengeza mawu a mfumu ndiponso lamulo lake, komanso atasonkhanitsa atsikana ambiri kunyumba ya mfumu ku Susani kuti Hegai aziwayangʼanira,+ Esitere nayenso anatengedwa kupita kunyumba ya mfumuyo kuti azikayangʼaniridwa ndi Hegai amene ankayangʼanira akazi.