-
Yeremiya 32:17-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 “Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Inuyo ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanu zazikulu+ ndi dzanja lanu lotambasula. Palibe chimene chingakuvuteni. 18 Inu amene mumasonyeza anthu masauzande ambiri chikondi chokhulupirika koma mumabwezera kwa ana,* zolakwa za abambo awo.+ Inu ndinu Mulungu woona, wamkulu ndi wamphamvu ndipo dzina lanu ndinu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 19 Zolinga zanu ndi zazikulu ndipo zochita zanu ndi zamphamvu.+ Maso anu amaona zonse zimene anthu amachita,+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zochita zake.+
-