3 Inu Yehova, kodi si paja maso anu amayangʼana anthu amene ndi okhulupirika?+
Mwawalanga koma sanamve kupweteka.
Ngakhale kuti munatsala pangʼono kuwawononga onse, iwo sanaphunzirepo kanthu.+
Anaumitsa kwambiri nkhope zawo kuposa thanthwe,+
Ndipo anakana kubwerera kwa inu.+