-
Aheberi 9:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Komabe, pamene Khristu anabwera monga mkulu wa ansembe wa zinthu zabwino zimene zakwaniritsidwa, anadzera mʼchihema chachikulu ndi changwiro kwambiri chimene sichinapangidwe ndi manja a anthu, kutanthauza kuti sichipezeka padzikoli. 12 Iye analowa mʼmalo oyera ndi magazi ake,+ osati ndi magazi a mbuzi kapena a ngʼombe zazingʼono zamphongo. Analowa kamodzi kokha mʼmalo oyerawo ndipo anatipulumutsa kwamuyaya.+
-
-
Aheberi 10:8-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Atanena kuti: “Nsembe zanyama, nsembe zopsereza zathunthu, nsembe zamachimo ndiponso nsembe zina simunazifune kapena kuzivomereza,” zomwe ndi nsembe zoperekedwa mogwirizana ndi Chilamulo. 9 Ananenanso kuti: “Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.”+ Akuchotsa dongosolo loyambalo kuti akhazikitse lachiwiri. 10 Tayeretsedwa ndi “chifuniro” chimenecho,+ kudzera mʼthupi la Yesu Khristu limene analipereka nsembe kamodzi kokha.+
-