Danieli 5:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 PERESI, ufumu wanu wagawidwa ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya.”+ Danieli 7:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ndinaonanso chilombo china chachiwiri, chooneka ngati chimbalangondo.+ Chinali chotukuka mbali imodzi ndipo mʼkamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake. Chilombochi chinauzidwa kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri.’+ Danieli 8:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Nditayangʼana ndinaona nkhosa yamphongo+ itaima pafupi ndi mtsinjewo ndipo inali ndi nyanga ziwiri.+ Nyanga ziwirizi zinali zazitali koma imodzi, imene inamera pomalizira, inali yaitali kuposa inzake.+ Danieli 8:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri imene unaona, ikuimira mfumu ya Mediya ndi mfumu ya Perisiya.+
5 Ndinaonanso chilombo china chachiwiri, chooneka ngati chimbalangondo.+ Chinali chotukuka mbali imodzi ndipo mʼkamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake. Chilombochi chinauzidwa kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri.’+
3 Nditayangʼana ndinaona nkhosa yamphongo+ itaima pafupi ndi mtsinjewo ndipo inali ndi nyanga ziwiri.+ Nyanga ziwirizi zinali zazitali koma imodzi, imene inamera pomalizira, inali yaitali kuposa inzake.+