-
Danieli 2:44, 45Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
44 Mʼmasiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa.+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa anthu a mtundu wina uliwonse.+ Koma udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa+ ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.+ 45 Zidzachitika mogwirizana ndi zimene munaona kuti mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu ndipo unaphwanya chitsulo, kopa, dongo, siliva ndi golide.+ Inu mfumu, Mulungu Wamkulu wakudziwitsani zimene zidzachitike mʼtsogolo.+ Maloto amenewa adzakwaniritsidwa ndithu ndipo kumasulira kwake nʼkodalirika.”
-