14 Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndidzaika magoli achitsulo pamakosi a mitundu ya anthu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya Babulo, ndipo akuyenera kudzamutumikira.+ Nebukadinezara ndidzamupatsanso ngakhale nyama zakutchire.”’”+