-
Yeremiya 27:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 ‘Ine ndi amene ndinapanga dziko lapansi, anthu ndi nyama zapadziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanga zazikulu ndiponso dzanja langa lotambasula. Ndipo dziko lapansili ndalipereka kwa amene ndikufuna.*+ 6 Tsopano ndapereka mayiko onsewa mʼmanja mwa mtumiki wanga, Mfumu Nebukadinezara+ ya ku Babulo. Ndamupatsanso ngakhale nyama zakutchire kuti zimutumikire. 7 Mitundu yonse ya anthu idzatumikira iyeyo, mwana wake wamwamuna ndi mdzukulu wake mpaka idzafike nthawi yoti ufumu wake uthe.+ Pa nthawi imeneyo, mitundu yambiri ya anthu ndi mafumu amphamvu adzamupangitsa kuti akhale kapolo wawo.’+
-