2 Kenako Mfumu Nebukadinezara inatumiza uthenga kwa masatarapi, akuluakulu a boma, abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu a zamalamulo ndi oyangʼanira onse a zigawo kuti asonkhane kumwambo wotsegulira fano limene Mfumu Nebukadinezara inaimika.