24 Taonani! Anthu abwera kumzinda uno ndipo amanga malo okwera omenyerapo nkhondo kuti aulande,+ moti uperekedwa mʼmanja mwa Akasidi amene akumenyana ndi anthu amumzindawu. Anthu adzafa ndi lupanga,+ njala ndi mliri.+ Zinthu zonse zimene munanena zachitika ndipo ndi izi mukuzionazi.