-
Deuteronomo 28:49-51Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
49 Yehova adzatumiza mtundu wakutali+ kuchokera kumalekezero adziko lapansi kuti udzakuukireni. Mtunduwo udzakuukirani mofulumira kwambiri ngati mmene chiwombankhanga chimagwirira nyama.+ Mtundu umenewo chilankhulo chake simudzachimva,+ 50 mtundu wooneka moopsa umene sudzamvera chisoni munthu wachikulire kapena kuchitira chifundo mnyamata.+ 51 Iwo adzadya ana a ziweto zanu ndi zipatso za nthaka yanu mpaka mutawonongedwa. Sadzakusiyirani mbewu iliyonse, vinyo watsopano kapena mafuta, mwana wa ngʼombe kapena mwana wa nkhosa mpaka atakuwonongani.+
-
-
Yeremiya 5:15-17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 “Ndikukubweretserani mtundu wa anthu kuchokera kutali, inu a mʼnyumba ya Isiraeli,”+ akutero Yehova.
“Umenewu ndi mtundu umene wakhalapo kwa nthawi yaitali,
Ndi mtundu wakale kwambiri,
Mtundu umene chilankhulo chake simukuchidziwa,
Ndipo simungamve zimene amalankhula.+
16 Kachikwama kawo koikamo mivi kali ngati manda otseguka.
Onse ndi asilikali.
17 Iwo adzadya zokolola zanu ndi zakudya zanu.+
Adzadya ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.
Adzadya nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu.
Adzadya mitengo yanu ya mpesa ndi mitengo yanu ya mkuyu.
Iwo adzawononga ndi lupanga mizinda yanu imene mumaidalira, yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.”
-
-
Yeremiya 6:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Yehova wanena kuti:
“Taonani! Anthu akubwera kuchokera kudziko lakumpoto.
Ndipo mtundu wamphamvu udzadzutsidwa kuchokera kumadera akutali kwambiri a dziko lapansi.+
23 Iwo adzagwira uta ndi nthungo.
Amenewa ndi anthu ankhanza ndipo sadzasonyeza chifundo.
Mawu awo adzamveka ngati mkokomo wa nyanja
Ndipo adzabwera pamahatchi.+
Iwo afola mwa dongosolo lomenyera nkhondo ngati mwamuna wankhondo kuti amenyane nawe, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni.”
-
-
Ezekieli 23:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Choncho iwe Oholiba, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndichititsa kuti amuna omwe unkawakonda,+ amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo akuukire. Ndidzawabweretsa kuchokera kumbali zonse kuti adzakuukire.+ 23 Ndidzabweretsa amuna a ku Babulo,+ Akasidi onse,+ amuna a ku Pekodi,+ a ku Sowa, a ku Kowa pamodzi ndi amuna onse amʼdziko la Asuri. Onsewa ndi anyamata osiririka, abwanamkubwa, achiwiri kwa olamulira, asilikali komanso amuna osankhidwa mwapadera.* Onsewa ndi akatswiri okwera mahatchi.
-